Kwelepeta adandaulira Nyumba ya Malamulo za kuchedwa kuwathandiza pa kusweka kwa galimoto lawo

Advertisement
Kwelepeta

Aphungu ochuluka achizimayi ndi ena aamuna Lero atuluka mnyumba ya Malamulo kuwonetsa mkwiyo wawo pomwe ati Nyumba ya Malamulo sikuwathandiza a Grace Kwelepeta omwe ndi phungu wa dela la Zomba Malosa ndipo galimoto lawo linabowoledwa mateyala ndi kuphwanyidwa nyali ndi anthu omwe ati anavala makaka a chipani cha Malawi Congress (MCP) mwezi watha.

A Kwelepeta omwe ndi phungu wa chipani cha Democratic Progressive (DPP) anayimanso mnyumbayi lero monga akhala akudandaulira sabata yonseyi, kufunsa sipikala kuti n’chifukwa chani sakuwathandiza pa nkhani ya kusakazidwa kwa galimoto lawo.

Wachiwiri oyamba wa sipikala a Madalitso Kazombo ati nkhaniyi ili m’manja mwa adindo a Parliamentary Service Commission ndipo athandizidwa.

Poyankhula ndi Malawi24, a Kwelepeta ati akuvutika mayendedwe pomwe ati akumachita kutengedwa ndi anzawo kupita ku zokambirana kunyumba ya Malamulo chichitikireni nkhaniyi.

Poyankhula Lero phungu wa Thyolo Central, a Ben Phiri ati ndi zomvetsa chisoni kuti kufikira lero nkhaniyi sinasongole pomwe nkhaniyi inachitika kalekale ndipo ikuthamangira kutha mwezi. Iwo anafunsa kuti kodi kukonza mavuto ngati awa zimatenga nthawi yayitali bwanji?

Galimoto la a Kwelepeta limodzi ndi la phungu wa Zomba Changalume a Lonnie Chijere idawonongedwa mwezi wa February ku Nyumba ya Malamulo komweku pomwe mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera anabweranso kunyumbayi kudzayankha mafunso kuchokera kwa aphungu.

Zimtepa za kunyumba ya Malamulo zomwe Malawi24 inawona zikuzungulira masamba a mchezo zidatepa anthu ena atazungulira galimoto za aphungu ndi ena amaoneka akubaya mateyala koma atavala makaka a chipani cha MCP.

Bungwe la Humans Right Defenders Coalition (HRDC) kudzera mwa wapampando wake a Gift Trapense adati ngati akupangidwa chipongwe aphungu kunyumba ya Malamulo, nanga kuli bwanji anthu wamba? ndipo adadzudzula mchitidwewu.