
Mtsogoleri wa chipani cha United Transformation Movement (UTM) a Dalitso Kabambe ati nthawi yakwana tsopano kuti masankho omwe akubwera pa 16 September 2025 aMalawi asayang’ane kwambiri ndale koma kusintha umoyo wa anthu kuti ukhale bwino posankha munthu amene akudziwa bwino za m’mene umoyo wa anthu ungachitire bwino komanso chitukukuko.
A Kabambe amayankhula Lachitatu m’boma la Karonga pa ulendo wawo obwelera kuchokera ku Chitipa ndipo ati aMalawi achita ndi kuvotera ndale kwambiri ndipo zafika potopetsa pomwe anthu ayesa zipani zina zomwe zayesapo m’mbuyomu ndipo zinakanika kufikira pa mlingo owamvetsa aMalawi bwino.
Iwo ati atsogoleri ambiriwa amangoyankhula za kusintha umoyo wa anthu koma ndalama samayidziwa ndipo masamu ake sangawatsate, ndipo ati atsogoleriwa samapeleka ndalama zokwana ku ma khonsolo ndipo ati iwo adzapeleka 100 billion Kwacha ku boma lililonse.
A Kabambe abwelezanso ndi kutsindika kuti adzaika ndalama zokwana 500 billion Kwacha ku ntchito zokopa alendo, ndi 500 billion ina ku ntchito za migodi mwa zina zomwe zidzalembe anthu ntchito, pomwe ati chipani cha UTM chikubwera kudzakonza chuma cha dziko lino kuti chikhale mchimake ndi kuthetsa tsankho pa chitukuko.
A Kabambe anatinso mtsogoleri wapakali pano a Lazarus Chakwera atopa ndipo anthu akufunika kuti mu September akawapumitse chifukwa zinthu zikuwavuta kwambiri mdziko muno.
Mtsogoleri wa UTM yu akamayenda misonkhano mwawo akumatsidzika pa kusintha kwa chuma cha dziko lino ponena kuti pamenepo ndi pomwe pagona gwero la kusintha kwa umoyo wa aMalawi.