Chakwera wadzudzula mchitidwe wa ziwawa

Advertisement
Chakwera

M’tsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera wadzudzula mchitidwe wa ziwawa omwe unachitika dzulo ku Lilongwe. Iwo apempha apolisi kuti afufuze mwansanga ndikuchitapo kanthu.

Kudzera mkalata yomwe yatulutsa nyumba ya chifumu ndipo yasayinidwa ndi m’neneri wa pulezidenti Anthony Kasunda, a Chakwera ati ndi okhudzidwa ndi mchitidwewu chifukwa kuchita zionetsero ndi ufulu wa anthu kotero kusokoneza ufuluwu ndikolakwika.

Kudzudzula kwa m’tsogoleri yu kukutsaria zomwe zachitika dzulo ku Lilongwe komwe anthu ena osadziwika anamenya ndi kutema anthu ogwira ntchito m’boma omwe amafuna kuchita zionetsero.

M’tsogoleriyu wachenjeza omwe akugwiritsa ntchito ndale kapena zionetsero pofuna kuyambitsa ziwawa, ponena kuti salola kuti ziipitse mbiri yabwino ya dziko lino mu Africa.