
Phungu wa Chitipa South Werani Chilenga yemwe wajoyina chipani cha Malawi Congress (MCP) posachedwapa akuti m’tsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera azawina ndi 70 pelesenti ndipo sakuwopa chipani cha DPP.
“Zomwe anthu akumakamba kuti palibe chipani chomwe chingapambane ndi 50+1 ndi zabodza, ndipo ndinene pano kuti Lazarus Chakwera azawina ndi 70 pelesenti,” atero a Chilenga.
A Chilenga atsutsanso zoti iwowo akufuna kubweletsa bilu ya zaka ku Nyumba ya Malamulo.
“Palibe akuwopa chipani cha DPP, ndipo a Chakwera sangasayinire bilu imeneyi,” iwo atero.
Dziko lino likuyembekezereka kuchititsa chisankho chapatu mmwezi wa September chaka chino, ndipo anthu adzasankha mtsogoleri wa dziko, aphungu ndi makhansala.