Walifwanthamula bodza: Chakwera anamiza a Malawi pa zitukuko

Advertisement
Malawi President Chakwera

Lero m’tsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera wavwavwaniza a Malawi ndi bodza lankunkhuniza ponena kuti boma lake lachita zitukuko za nkhani nkhani m’dziko muno zomwe ambiri akupukusa mutu opanda nyanga.

Chimodzi mwa zitukuko zomwe Chakwera anati boma lake lachita ndi kumanga nyumba za a polisi zokwana 24 m’boma la Likoma. Koma Malawi24 yapeza kuti m’bomali mulibe ngakhale nyumba imodzi yomwe yamangidwa.

Poti kutsutsa galu mkukumba, mai Ellen Longwe omwe amakhalira dera la Madimba pa chilumba cha Likoma, ati anadzidzimuka atamva Chakwera akuyankhula kuti boma lake lamanga nyumba zokwana 24 pa zilumbazo.

“Ndikutsimikizireni iwe mtolankhani kuti kuno nyumba akunenazo kulibeko mwina zinamila m’madzi nthawi yomwe anamanga,” watsutsa mwantu wagalu Longwe.

Nako Nsanje, Malawi24 yapeza kuti ntchito yomanga nyumba za apolisi ili pa maziko kumene (foundation). 

Wapampando wa khonsolo ya m’bomali, a Cassim Ussein Ngwali, wati, zomwe akudziwa mzakuti ntchito yomanga nyumba 28 za apolisi yangoyamba kumene, palibe nyumba yomwe yatha. 

Malingana ndi a Ngwali nyumba khumi akuzimanga ku polisi ya Chiromo ndipo 18 ku polisi ya Marka. Kampani ya Tapita ndi yomwe ikugwira ntchitoyi. 

Izi zikusiyananso ndi zomwe m’tsogoleri wa dziko linoyu, walankhula m’nyumba ya malamulo lero kuti boma lake lamanga nyumba 28 m’bomali za ogwira ntchito ya chitetezo mwazina ati pofuna kulimbikitsa chitetezo m’bomali.