Apha munthu chifukwa cha thelere

Advertisement
Malawi24

Apolisi m’boma la Mulanje akhazikitsa ntchito yosakasaka munthu yemwe akumuganizira kuti wapha mzake atamugwira akuba therere m’munda mwake.

Mneneri wa apolisi m’bomali, Innocent Moses, wati izi zachitika usiku wa Lamulungu m’mudzi mwa Gojo kwa mfumu Mthiramanja.

“Thupi la Piyasi Ligomeka linapezeka m’munda lili ndi mabala aakulu. Woganiziradwayu anabwereka munda wa wophedwayu ndikubzalamo therere logulitsa. Ndipo Lamulungu anapita ndi mnzake kokalondera mundawo atazindikira kuti anthu akumamubera therere lake,” iye watero.

Moses wati anthuwa anagwira Ligomeka m’mundamo ndipo anamumenya n’kumusiya atakomoka ndipo anakanena za izi kwa Nyakwawa Gojo.

Iye wati: “Lolemba, abale ake a Ligomeka anayamba kumusaka pozindikira kuti sanabwere kunyumba ndipo anampeza m’munda. Zotsatira za kuchipatala zawonetsa kuti Ligomeka wafa kamba kotaya magazi komanso kumenyedwa kwambiri.”

Pakadali pano, oganiziridwawa athawa ndipo apolisi akuwasaka kuti awamange n’kukayankha mlandu wakupha.

Apolisi alangiza anthu kupewa kutengera malamulo m’manja mwawo, ponena kuti kutero ndi kuphwanya malamulo.