Alekeni aMalawi asankhe yemwe akufuna – Kachamba

Advertisement
Malawi Politics

M’modzi mwa ochita malonda m’dziko muno, Kondwani Kachamba walakhurapo za bilu yomwe ikufuna kupita ku Nyumba ya Malamulo yoletsa munthu yemwe wafika zaka 80 kuyimira pa udindo wa m’tsogoleri wa dziko.

Polankhura pa tsamba lawo la mchezo, a Kachamba ati aliyense kaya wa zaka 90, kaya 60, kaya 39 ndi m’Malawi, ndipo awasiye aMalawi asankhe yemwe akufuna kumtima kwawo.

A Kachamba akuti zawonekeratu kuti bilu imeneyi ndiyofuna kulimbana ndi APM, ndipo ambali inayo akuyesetsa njira zonse kuti amulepheretse APM kuyimira nawo pa zisankho.

Kondwani_Kachamba
Kachamba: Biluyi yabwera mu nthawi yolakwika.

“Koma chilungamo chake ndi chakuti APM ndiye chisankho cha anthu ambiri m’dziko muno pa anthu onse omwe akuyimira pa udindo wa m’tsogoleri wa dziko. Pangani kampeni, bweletsani fundo ndipo munthu yemwe aMalawi amukonde azawina zisankho,” iwo anatero.

Kachamba anapitiliza kunena kuti anthu ena azimutchula kuti ndi cadet koma zomwe wakambazo ndi chilungamo.

“Akufuna kuletsa chisankho cha anthu, anthutu amakhala ndi zokonda zosiyanasiyana. Malawi ngwatonse, tivomereze nthawi yobweletsa bilu yi ndi yolakwika,” anatero Kachamba.

Malingana ndi a Kachamba bilu yi yabwela nthawi yolakwika chifukwa kwangotsala miyezi yochepa kuti tipite ku chisankho ndipo ena omwe akuyimira ali ndi zaka zodutsa 80 zomwe owatsatira awo alibe nazo vuto.