Ndidakuuzani lero ndi izi, wayankhula Usi pakusavana ku UTM

Advertisement
Usi

Mawu akulu akoma akagonera! Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Michael Usi, wasambira m’manja akuluakulu a chipani cha United Transformation Movement (UTM) pachipwilikiti chomwe chabuka m’chipanichi ponena kuti iye adawachenjeza kale konveshoni isanachitike.

Usi wayankhula izi Lamulungu pomwe anakumana ndi anthu otsatira chipani cha UTM omwe anachokera ku Ndirande. Anthuwa anakhamukira ku nyumba ya Usi ku Mudi munzinda wa Blantyre komwe akuti amakatula nkhawa zawo.

Poyankhula ku khwimbiri, Usi wati, “Komatu ine ndidanena kuti izi mukupanga apazi mulira. Make njiwa adamuuza mwana njiwa kuti usadutse uku, koma mwana njiwa adakakamira pamapeto pake mwana njiwa adabwera akulira. Inetu a Chilima ndidagwira nawo ntchito limodzi, ndimaona zimene akufuna, ndimawelenga zonse nde ndimawauza abale angawa mokoma mtima kuti izi mulira koma amapanga makani, lero kuli bwino?”

Iwo anapitilira ndikufotokoza mkuluwiko wakuti “Chinthu chikakhala chako ngakhale chisali ndiiwe chimakhala chakobe basi, ndiponso chinthu ngati sichako ngakhale chili ndi iwe sichakobe.”

Usi wati akukonza tsiku loti ayankhule anthu omutsatira pa za tsogolo lake ku chipani cha UTM komanso tsogolo lake pa ndale. Iye wati pakadali pano watanganidwa ndikuwonetsetsa kuti anthu m’dziko muno ali ndi chakudya.

Izi zikubwera pomwe zikuoneka kuti mchipani cha UTM mwabuka kusavana chifukwa cha zotsatira za chisankho cha mtsogoleri wa chipanichi ku konveshoni yapitayi. A Patricia Kaliati, Newton Kambala komaso Matthews Mtumbuka abwera poyera ndikuwulura kuti akuganizira kuti panali zachinyengo pa chisankhochi.

Advertisement