Amemeza anthu kukalembetsa mkaundula wa mavoti

Advertisement
Zomba

Pomwe pangotsala masiku awiri kuti gawo lachiwiri lakalembera wachisankho lithe, yemwe akufuna kuzayimira ngati phungu wakunyumba yamalamulo muchipani cha MCP m’dera lakumwera mu nzinda wa Zomba, Patricia Kainga Nangozo, wapempha anthu amdelari omwe sadalembetsebe kuti apite akalembetse.

Nangozo wapempha anthu amdera lakumwera mumzinda’wu kuti akalembetse mwaunyinji kuti adzathe kuvotera iye ngati phungu wakunyumba yamalamulo komanso adzavotere a Lazarus Chakwera ngati mtsogoleri wadziko lino pachisankho cha chaka chamawa cha 2025.

Iye wati kusalembetsa kalembera wachisankho zikutanthauza kuti sudzaponya nawo voti pachisankhochi komanso zikutanthauza kuti sumafunira dziko lako zabwino pankhani yachitukuko.

Pamenepa, Kainga Nangozo wati ngati anthu amdera lakum’mwera mumzinda wa Zomba akufuna chitukuko chamiseu yamakono, magetsi, sukulu, madzi okumwa a ukhondo komanso kutukula amai ndi achinyamata pankhani za bizinesi ayenera adzamusankhe iye kukhala phungu.

“Ndidakhalapo mbuyomu phungu wamdera lapakati mu mzinda wa Zomba choncho ndikuziwa pomwe ndidalekezera pankhani yachitukuko ndiye muzandisankhe kuti ndizapitilize ntchito zamanja anga,” iwo anatero.

Bungwe lowoona zachisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) likuyembekezeka kuzachititsa chisankho chapatatu chosankha mtsogoleri wadziko, aphungu akunyumba yamalamulo komanso makhansala chaka chamawa cha 2025 ndipo padakali pano kalembera wachisankhochi adayamba.

Advertisement