Pakutha pankumano omwe anayitanidwa ndi mkulu wa bungwe la MERA Henry Kachaje, mkulu wa bungwe la CDEDI, Sylvester Namiwa wati zikuoneka kuti vuto la kusowa kwa mafuta a galimoto lipitilirabe ponena kuti naye Kachaje alibe chiyembekezo pa tsiku lenileni lomwe vutoli lingathe.
Kachaje anayitanitsa akuluakulu a bungwe la Centre for Democracy and Economic Development Initiatives ku nkumano komwe amakafotokoza zomwe bungwe la MERA likuchita pofuna kuthana ndi vuto la mafuta a galimoto lomwe lafika sabata yachisanu tsopano.
Poyankhula kwa atolankhani utatha nkumanowu, Namiwa anati “Takumana nawo a Kachaje, anayesera kuti afotokoze zomwe zikuchitika koma ah mavuto alipo ndithu. Naye alibe chiyembekezo ndipo alibe mayankho pa mavutowa. Momwe tawamvera, mavuto akanalipo. Ndiye tawauza pamaso pawo kuti bola angotula pansi udindo wawo pabwere ena agwirepo ntchito.”
Pa nkhani yoti Kachaje akugwira ntchito yake ku MERA chonsecho kontalakiti yake idatha, Namiwa wati: “Tinawafunsa izi kutsatira zoti iwo kontilakiti yawo inatha mu August, ndiye anakana kuyankhapo za izi. Anangoti sakufuna kuyankhapo kanthu.”
A Kachaje anayitanitsa nkumanowu potsatira zionetsero zomwe bungwe la CDEDI CDEDI lalengeza kuti lichititsa Lachinayi lino pofuna kukamiza adindo kuti achitepo kanthu pa vuto la kusowa kwa mafuta a galimoto m’dziko muno.
Bungwe la CDEDI motsogozedwa ndi Namiwa, likufuna nduna ya za mphamvu a Ibrahim Matola komaso a Kachaje atule pansi udindo wawo ponena kuti alephera kuthana ndi vuto lakusowa kwa mafutali.