Malawi yapatapo Point yoyamba, Pasuwa wayamba kulandira muyeso wake

Advertisement
Flames

Atachita ma pulakatesi panja pa Radisson Blue hotel kukonzekera masewelo mu 2025 AFCON Qualifier ndi Burundi pa bwalo la Felix Houphouet Boigny in Abidjan, mdziko la Ivory Coast, lero Malawi yapatapo point yake yoyamba chiyambireni mpikisanowu.

Masewelawa omwe anayamba 5 koloko madzulo lero, Calisto Pasuwa yemwe ndi m’phunzitsi wa timuyi ndi omuthandizira ake, Peter Mponda ndi Richard Mwansa, anayambitsa masewerowa mwachilendo mosiyana ndi momwe analili Mabedi. William Thole pa golo, McDonald Lameck, Charles Petro, Denis Chembezi, Richard Mburu, Gabadibho Mhango , Alick Lungu, John Banda,, Gaddie Chirwa , Lanjesi Nkhoma ndi Yankho Singo.

M’chigawo choyamba Malawi inasewela bwino ndi kupata mwayi oti ikhonza kutsogola koma sizinatheke.

Chigawo choyamba chomwe Malawi inasewela mwa pamwamba kwambiri ndi kupeza mipata ingapo chinathera 0-0 awiriwa atalumilana mulomo wapansi.

Pasuwa anayesa kulowetsa anyamata monga Lloyd Aaron, Chawanangwa Kaonga, Wisdom Mpinganjira, Gomezgani Chirwa, kuti mwina m’kupeza ma point onse atatu koma sizinachitike chifukwa anyamata a Burundi anakhoma khoma lomwe Gaba ndi anzake amakanika kugumula.

Ataonjezera Mphindi zinayi oyimbila anaweluka kuti palibe yomwe yapambana koma kugawana ma point, Malawi yapatapo point yake yoyamba chiyambireni masewero ake mu AFCON qualifiers.

Advertisement