Chakaka chisembwere ku boma: wamkulu wa boma aphwanyiridwa galimoto kopakula

Advertisement
Thabo Chakaka Nyirenda

Galimoto ya boma yomwe amayendera mkulu wa za malamulo mu boma a Thabo Chakaka Nyirenda yaswedwa dzulo mu Lilongwe.

Malinga ndi malipoti, bambo wina wokwiya dzulo usiku anatengera yekha malamulo m’manja ndi kuswa galimoto loyendera bambo Chakaka ati chifukwa akhala akusokoneza banja lake.

Bamboyu, a Harris Nantikwa, analemba pa tsamba lawo la mchezo la Facebook kuti a Chakaka akhala akugona ndi mkazi wawo kwa kanthawi mpaka anapangitsa mkaziyo kupita ku bwalo kufuna kuthetsa ukwati.

“Thabo Chakaka Nyirenda wakhala akundidyera kwa ka nthawi ndithu, mpaka mkazi kupita ku bwalo kuti tisiyane. Nkhani koma kumeneko nayo sikusuntha. Ine mpaka pano ndinaletsedwa kukafika kunyumba kwathu ndi a bwalo amene anatsogozedwa ndi bambo opusa uyu Chakaka,” analemba mwa ukali choncho a Nantikwa.

Malawi AG Car

Iwo anapitirira kulira kuti abwela ndi nkhaniyi kugulu kupangira kuti a Malawi adziwe kuti akachitidwa chipongwe amene angakhale wawachita chotero ndi bambo Chakaka Nyirenda.

“Amachita kubwera ku nyumba kwanga mkati mwa usiku ndi kuzasangalatsana ndi mkazi wanga pa bed langa lomwe,” analira motero bamboyo.

Zikuoneka kuti mu chidimadima cha mkwiyo bamboyu anangoganiza zokuswa galimoto ya boma yomwe amayendera a Chakaka.

Advertisement