A Chakaka Nyirenda atule pansi udindo – yatero CDEDI

Advertisement

Bungwe lolimbikitsa chilungamo komanso kuunikira momwe Boma likuyendera la Centre for Democracy and Economic Initiatives (CDEDI) lati mlangizi wa boma nkhani za malamulo (Attorney General) Thabo Chakaka Nyirenda atule pansi udindo ngati sapereka umboni pa za ndalama yokwana K750 Million ya ndondomeko ya zipangizo za ulimi zotsika mtengo (AIP) yomwe inalipilidwa kwa ochita malonda ogulitsa nyama wa ku Mangalande.

Poyankhula pa mkumano wa atolankhani ku Lilongwe, Mkulu wabungweli Sylvester Namiwa wati  iwo akukhulupirira kuti polimbikitsa mlangizi wamkulu wa boma pa malamuloyu  kuuza a Malawi za nkhaniyi sakufunsa zambiri, chifukwa izi ndizomwe  analonjeza okha m’mwezi wa Disembala chaka chatha kuti adzachita.

A Namiwa ati polankhula ndi wailesi ya Times m’mbuyomu a Nyirenda  anachita kunena okha  kuti ndiwokonzeka kutula pansi udindo ngati ndalamayi siyitoleredwa yonse.

Iwo awonjezera kuti Mlangizi yu anawuza dziko lino kuti anapitapo ku dziko la Germany kuti akatolere gawo  lina la ndalamazi zomwe zinali ku banki ina mdzikolo.

“Lero patatha miyezi inayi, CDEDI pogwiritsa ntchito lamulo la kapezedwe ka nkhani la Access to Information (ATI) likukumbutsa mlangizi wa boma pa

malamuloyu za nkhani yofunikirayi ku dziko lino. Ndizosakayikitsa kuti a Malawi ali tcheru kudikirira kumva kuti ndi ndalama zingati zomwe zatoleredwa

ku K750 miliyoni.

“Ndichachidziwikirenso kuti chiyembekezo cha aliyense ndikufuna kuona kuti ndalama yonse yatoleredwa. Mlangizi wa boma pa malamuloyi, akuyenera kufotokozeranso a Malawi kuti ndi chifukwa chani kupatula kuchotsedwa ntchito kwa nduna ya kale ya zaulimi a Lobin Lowe ndi wachiwiri wawo a Madalitso Kambauwa Wirima, palibe yemwe anamangidwapo pokhudza nkhaniyi,” afotokoza motero  Namiwa.

Mkulu wa CDEDI yu wanenanso kuti nchachidziwikire kuti cholinga cha ndalamayi chinali kufuna kupulumutsa a Malawi ovutikitsitsa ku njala, choncho ndichifukwa chake nkhaniyi  siyingangokwiriridwa.

Iwo ati Mlangizi wa boma pa malamuloyu akungoyenera kunena chilungamo pa za nkhaniyi kuphatikizaponso cholinga cha maloya omwe anati anaperekako gawo lina la ndalamayi.

“Akakanika kutero, iwo angotula pansi udindo modzichepetsa monga mwa lonjezo lawo.

“Poonjezera, CDEDI ikufuna mlangizi wa boma pa malamuloyu achitepo kanthu pa zakusowa kwa ziphaso zoyendera kapena kuti mapasipoti. Mongofanananso ndi nkhani ya zipangizo za ulimi zotsika mtengo (AIP), mlangizi  wa boma pa malamuloyu anatsimikiziranso nyuzipepala ya pa makina a intaneti  ya Nyasa Times pa 23 Febuluwale, 2023 kuti a Malawi asade nkhawa pa za  nkhani ya kupezeka kwa mapasipoti. Koma pakadali pano zinthu  zasokonekeratu ku nthambi yoona zolowa ndi kutuluka (Immigration),” atero a Namiwa

Pomaliza  a Namiwa ati molingana ndi nkhani ziwirizi, CDEDI yapereka sabata imodzi kwa mlangizi wa boma pa malamuloyu kuti ayankhepo ndipo adziwe kuti akapanda kutero, iw adzachita m’bindikiro pa chipata cholowera ku ofesi yawo ku Capital Hill.

Follow us on Twitter:

Advertisement