Samalani ana mu nyengo ya mvula – Makolo achenjezedwa

Advertisement
Mzimba

Ofesi yowona za chisamaliro cha anthu m’dera la kum’mwera kwa boma la Mzimba yalangiza makolo ndi alezi kuti pamene tikuyandikira nyengo ya mvula  makolo akuyenera kumaperekeza ana awo ku sukulu kupewa ngozi zomwe zingadze kamba ka nyengoyi

Mkulu wowona za chisamaliro chawanthu m’derali, Benard Nangwale, wati makoro akuyenera kuonetsetsa kuti ana komanso okalamba sakuyenda okha nthawi ya mvula.

Poyankhula ndi Malawi24, Nangwale wachenjeza makolo onse omwe amasiya ana awo opanda chithandizo.

“Ofesi yathu tsiku ndi tsiku tikulandira madando okhuza azibambo kulekelera mawanja awo zomwe zikupangitsa kuti ana ena azisiyila sukulu panjira, ndi chenjeze pano kuti ofesi yathu sitilekelera mchitidwe umenewu kuti udzikula. Makolo ali ndi udindo wosamala ma wanja awo, anatero Nangwale

Yemwe akuyang’anira zintchito ku bungwe la Mzimba Institute for Development Communication Trust-MIDCT Justice Nantchengwa wati akugwirizana kwa thunthu ndizomwe anena a Ngwale.

“Ife ngati bungwe titengapo gawo po kumbutsa anthu pogwiritsira njira zathu zomwe tinakhazikitsa ndi cholinga chakuti nkhani za chisamaliro cha ana, okalamba ziziyenda bwino,”atero a Nantchengwa

Ana ambiri mu boma la Mzimba akusowekera chithandizo angakhale kuti makolo awo alipo, kamba ka a bambo omwe anatayilira ma wanja awo.

A nthambi yoona za nyengo m’dziko muno alengeza pomwe anali ku Mzimba kuti bomali ilandira mvula yochuluka  chaka chino yomwe itsagane ndi mphepo ya mkuntho komanso ndi kusefukira kwa madzi madera ena.

Advertisement