Okuba chifanifani cha Mayi Maria agamulidwa kukakhala ku ndende zaka zisanu ndi chimodzi

Advertisement
Zomba

Bwalo lamilandu la Domasi ku Zomba lagamula a Madalitso Komwa kuti apite ku Ndende ndikukagwira ukaidi wakalavula gaga kwa miyezi 72 (zaka 6) chifukwa chomupeza olakwa pamulandu otchola ndi kuba chithunzi cha Amai Maria ndi zinthu zina mu church champingo wakatolika cha Katamba Parish mu Diocese ya Zomba.

Wapolisi oyimira Boma pamilandu Sub Inspector Peter Sosola adapempha bwalo kuti lipereke chilango chokhwima kwa wopalamulayu chifukwa mulandu omwe adapalamula udali waukulu komanso zomwe adachita ndizotsemphana ndi gawo 311 la buku lamalamulo oyendetsera milandu ya upandu.

A Sosolo adauzanso bwalo kuti lipereke chilango chokhwima popeza wopalamulayu kupalamula uku ndikachiwiri chifukwa mbuyomu adamangidwaponso miyezi 42 pamulandu wina otchola nyumba ndikuba.

Popereka chigamula chake oweruza milandu a Eric Mchosa adagwirizana ndi wapolisi oyimira Boma pamilandu kuti mulandu omwe adapalamula Madalitso Komwa ndiwaukulu komanso milandu yotchola nyumba ikuchulukira mdera la Domasi.

Pamenepa a Chosa adagamula kuti Komwa akakhale ku Ndende ndikukagwira ukaidi wakalavula gaga kwa zaka zisanu ndi chimodzi kuti anthu ena atengerepo phunziro.

A Komwa ndi a zaka 32 zakubadwa ndipo amachokera mudzi wa Mkumbira mdera la T/A Nkagula Boma la Zomba

Advertisement