Atolankhani angapo aphedwa ku Lebanon pomwe asilikali a dziko la Israeli akupitiliza kuponya mizinga ku delaro.
Kuphedwa kwa atolankhaniwo kwadza patatha masiku angapo Israeli itadzudzula atolankhani a kanema ya Al Jazeera ku Gaza ponena kuti atolankhaniwo akugwirizana ndi Gulu la Hamas
zomwe anthu ambiri ati ndizopanda pake.
Mizinga ina inalenga dera lina ku Lebanon komwe atolankhani 18 ochokera m’nyumba zosindika ndi kuulutsa mau zisanu ndi ziwiri (7) akukhala.
Mizingayo yawononga nyumba ndi magalimoto omwe atolankhaniwo amagwiritsa ntchito.
Nduna yofalitsa nkhani ku Lebanon, Ziad Makary, yadzuzula dziko la Israeli kamba koombera atolankhaniwo.
Pafupifupi atolankhani 128 akuti aphedwa kuyambira pomwe asilikali a Israeli anayamba kuthira nkhondo ku Gaza, West Bank, ndi Lebanon.
Maiko ambiri komanso mabungwe owona ma ufulu aatolankhani monga la Committee to Protect Journalists (CPJ) lomwe lili ku New York m’dziko la America lati zomwe likupanga dziko la Israeli kupha atolankhani ndi mtopola waukulu zomwe zikufunika kuti maiko onse adzudzule dziko la Israeli.