Bullets yafa ndi imodzi pomwe Wanderers yasaina Kamwendo

Advertisement
Promise Kamwendo

Pomwe timu ya FCB Nyasa Big Bullets inali itapeleka kale K3 miliyoni ndipo imadikira kuti iwonetse kugulu katswiri wosewera kutsogolo mu timu ya Premier Bet Dedza Dynamos, Promise Kamwendo, osewerayu watikitira kontalakiti ku Mighty Mukuru Wanderers.

Kamwendo yemwe lero Lolemba dzina lake linali pokopoko m’masamba a mchezo, wasayinira kontalakiti ya zaka zitatu ku Manoma ngakhale kuti timu ya Bullets inali itamvana kale ndi Dedza ndipo chomwe chinatsala ndikupezeka kwa osewerayu ku ma ofesi a timuyi.

 Tsamba lino lapeza kuti mwini wake Kamwendo ndiyemwe wapanga chiganizo cholowera ku Lali Lubani pamwamba pa Maule komanso Silver Strikers kamba kachithumba chomwe chinakhuthilidwa kwa m’nyamatayu.

Osewerayu akuti anatengedwa m’bandakucha wa Lolemba ku Dedza ndi yemwe amayang’anira osewera ku Wanderers Steve Madeira omwe amadziwika bwino pa nkhani yozembetsa osewera nthawi yomwe msika ogula ndi kugulitsa osewera ukatsegulidwa.

Mwachitsanzo, anazembetsapo Blessings Tembo, Jafali Chande ndi ena angapo.

Pakadali pano, Bullets sinaikepo ndemanga pa nkhaniyi. Chakumasanaku, Bullets yaonetsa kugulu osewera wa Dedza Lameck Gamphani ponwe wasainila mwirizano wa zaka zitatu.

Advertisement