Boma la Rwanda litseka kachisi oposera 4,000

Advertisement
Rwanda

Boma la Rwanda lati latseka makachisi oposera 4,000 ati kaamba kopemphelera mu malo a umve komanso kugwilitsa ntchito zimkuza mawu zomwe zimachita phokoso losaneneka.

Malingana ndi malipoti a nyumba yofalitsa nkhani ya BBC, zipembedzo zomwe zakhuzidwa ndi za chi pentekositi komanso chisilamu.

Nduna yowona za maboma ang’ono m’dziko la Rwanda, Jean Claude Musabyimana wati boma la dzikolo lachita izi pofuna kulimbikitsa bata m’dzikolo komanso chitetezo cha opembedza.

“Sitinapange chiganizochi pofuna kuletsa anthu kupemphera koma tikufuna kulimbikitsa chitetezo cha opembedza komanso bata,” idafotokoza ndunayi.

Mchaka Cha 2018, dziko la Rwanda lidakhazikitsa lamulo loti m’busa aliyense m’dzikolo azikhala ndi maphunziro a ukachenjede a utumiki.

Izi zidapangitsa kuti kachisi okwana 700 atsekedwe m’dzikolo.

Advertisement