Anthu akugwilitsa ntchito mapulasitiki pomwe makondomu akusowa ku Likoma

Advertisement
Likoma Island

Pali chiopsyezo kuti chiwerengero cha anthu otenga ka chirombo ka HIV komaso matenda ena opatsilana pogonana chitha kukwera m’boma la Likoma komwe anthu akugwiritsa ntchito mapulasitiki pogonana kamba koti makondomu akusowa.

Izi ndi malingana ndi nyuzipepala ya Nation yomwe yatulutsidwa lero Lamulungu ndipo yati anthu m’bomali nthawi zambiri akhala akupita kuchipatala kuti akatenge makondomuwa koma akumapeza kuti kulibe.

“Anthu ena amafuna chithandizo mwachangu choncho ngati kuchipatala kulibe makondomu, pamakhala mavuto akulu chifukwa anazolowera kulandira aulere chifukwa m’masitolo akumadula. M’malo mwake, ena akumagwiritsa ntchito ma pulasitiki,” watelo munthu wina yemwe wayankhula ndi nyuzipepala ya Nation.

Nyuzipepalayi yati wofalitsa nkhani zaumoyo pa chipatala cha m’bomali a Jomo Sumani avomereza kuti vutoli lilipodi ndipo ati izi zili chonchi kamba ka vuto la mayendedwe.

Iwo ati, “Musaiwale kuti pano ndi pa chilumba ndipo mayendedwe nthawi zina amavutirapo. Choncho ngati makondomu atha nthawi imene ife tikudikira kuti unduna wa zaumoyo m’nthambi ya HIV/Aids utipatse, timapempha m’zipatala zina monga cha Mzimba, koma chifukwa cha mayendedwe, zimatenga nthawi.”

Izi zikuyika anthu ochuluka m’bomali makamaka amayi ogulitsa matupi pa chiopsyezo choti atha kutenga ka chirombo koyambitsa matenda a Edzi komaso matenda ena opatsirana pogonana.

Advertisement