Phungu aphwanya pangano pa kalipilidwe ka antchito ake

Advertisement
Yeremiah Chihana

A Yeremiah Chihana omwe ndi phungu wa m’dera la kumpoto m’boma la Mzimba adandaulidwa ndi anthu 24 omwe amawagwirila ntchito kamba koti anaphwanya pangano la ndalama zomwe amayenera kuwalipira.

Anthuwa omwe pakadali pano akuswera pa ofesi ya za ntchito m’bomali ayenda mtunda wa makilomita 80 kuchokera ku Geza Mbalachanda pomwe akuyesetsa kupeza mayendedwe obwelera ku Mchinji.

Malingana ndi m’modzi mwa anthuwa Liviness Chayera auza Malawi24 kuti iwo powatenga anthuwa anauzidwa kuti azikalandira ndalama zokwana 4,500 kwacha patsiku koma atafika pa malo a ntchitowo anauzidwa kuti azilipilidwa 3000 kwacha patsiku. 

Mai Liviness atinso anali odabwa pa tsiku lachitatu atauzidwa ndi Mai Brenda Chihana omwe ndi mkazi wa a Yeremiah Chihana kuti malipilo awo asintha ndipo tsopano azilipilidwa 2000 kwacha pa tsiku.

“Tinayesetsa kuti tikambirane nawo bwana Chihana pankhani ya malipilo athu koma chodabwitsa iwo anatiuza kuti ngati sitikufuna kugwira ntchito tizipita kwathu, kutengera ndi ntchito yomwe timagwira malipilo sanali okwanira ndipo tinaganiza zoti tizibwerera kwathu , tagwira ntchito kwa masiku okwana asanu ndi atatu (8) ndipo tinapatsidwa ndalama yokwana 10,000 Kwacha aliyense,” atero mai Liviness.

Titayesera kuwayimbira lamya Kuti timve mbali yawo, a Yeremiah Chihana sanayankhe.

Wapampando wa mabungwe omwe asali aboma ku Mzimba Christopher Melele wati ndi zomvetsa chisoni kuti anthu omwe amapanga malamulo adzimveka ndi mbiri za mtundu oterewu. 

“Ife ngati a mabungwe ndife wokhudzidwa kwambiri kuti anthu akuphwanyilidwa ma ufulo awo mwa mtundu otere, pano chomwe tikupanga ndikuonetsetsa kuti anthuwa apeze chakudya komanso kuti abwelere kwao ku Mchinji,” atero a Melele

Iwo atinso ayankhulana kale ndi a phungu akunyumba ya Malamulo am’madera omwe anthuwa akuchokera pankhani ya mayendedwe.

Advertisement