Anthu akukonda Chakwera panthawi yokhayo apatsidwa maudindo  

Advertisement
Lazarus Chakwera

Wa pampando wa chipani cha Malawi Congress (MCP) mchigawo chapakati a Patrick Zebron Chilondola ati anthu ambiri akulemekeza mtsogoleri wa dziko lino akapatsidwa udindo koma akalandidwa udindowo mpamene amanyoza mtsogoleri wa dziko.

Poyankhula pa Mtengowanthenga m’boma la Dowa a Chilondola ati anthu ena adalandidwa unduna ndi ma udindo ena ndi chifukwa chake akunyoza a Chakwera lero ndi kumasocheletsa anthu.

“Mukafuna kusintha nduna mudzisintha m’mene mwafunira,” anatero a Chilondola.

A Chilondola ati zipani zina zikungolalata m’masamba a mchezo ndipo adzudzula anthu ena omwe masiku apitawa amalankhula mwa mtudzu ku misonkhano ya ku Mzuzu ndi Mangochi.

A Chakwera anayima pamalopa mu ulendo wawo opita ku Mzuzu lero.

Advertisement