Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Micheal Usi ati mzosabisa kuti ogwira ntchito ena m’boma akugwira monyentchera kotero mkoyenera kuwachotsa ntchito kuti dziko lidziyenda.
Poyankhula lamulungu m’mudzi mwa a Golden m’boma la Mulanje, a Usi ati ogwira ntchito ena m’boma amangokhalira ma pepala a zinthu zofunika kuthandiza anthu amene akuvutika ku midzi pamene ena ndi ongochita zinthu kuti atsogoleri awoneke oyipa kotero kuti oterowa si ofunika pa malo.
Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dzikoyu watsindikanso kuti m’mwezi wa July ndi August anthu alandira ndalama za ngongole zopanda chikole kwa anthu ovutika mosayang’anira mtundu, chipani kapena dela.
Pa msonkhanowu a Usi anadzitalikitsila okha ndi chipani chilichonse ponena kuti kutumikira kwawo ndikwa zipani zonse.
“Musamandizunguze ndi nkhani za chipani, mumfune; ine khumbo langa ndi kutsogoza miyoyo ya anthu chifukwa pamapeto mudzaloza ine, ndipo onse onditukwana mulungu awakhululukire” anatelo a Usi polankhula.
Iwo alonjezanso kuti mwa iwo okha akhala akugawa zakudya kwa okalamba m’madela ena kudzera mu thandizo lomwe apempha kwa ena akufuna kwabwino ochokera m’maiko a kunja.
Mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera sabata latha ku Lilongwe adalankhulanso kuti Malawi akuyenda pang’ono pang’ono m’chitukuko chifukwa pali ena m’boma amene amadzinamiza kuti dziko lino lili ndi nthawi yokwanila.