Mtsogoleri wa dziko la America Joe Biden wapezeka ndi Covid-19

Advertisement
Biden

Mtsogoleri wa dziko la United States of America, Joe Biden amupeza ndi Covid-19 Lachitatu. 

Izi zikudza patangodutsa nthawi yochepa chabe mtsogoleriyu chinenereni kuti sazayimira nawo pa zisankho zili mkuza ngati madotolo adzamupeze ndi vuto lalikulu. 

“Andipeza ndi Covid-19 madzulo ano, koma ndikupeza bwino ndipo ndikuthokoza aliyense amene amandifunira zabwino.

Ndikhala kodzipatula pamene ndikuyembekeza kuti ndikhale bwino konse, munthawiyi ndipitliza kugwira ntchito kuonetsesa kuti zonse zikhale nchimake kwa mzika za ku America,” anatero Biden kudzera pa tsamba lake la Twitter. 

Biden, yemwe padakali pano ali ndi zaka 81 zakubadwa, ndi m’tsogoleri wa nambala 46 ku America ndipo anatenga boma  mu chaka 2021 ndipo akuyembekezeka kudzayimira mu zisankho zomwe zichitike mu November chaka chomwe chino. 

Izo zili chomwecho, malingana ndi tsamba la CNN, kufikira pa 6 mwezi uno muliri wa Covid-19 unakwera ndi pafupifupi 24% ku America. 

Advertisement