Ngalawa zikuduphidwa! Kabambe atuluka DPP

Advertisement
Kabambe

A Dalitso Kabambe omwe anaonetsa chidwi chokapikisana nawo pa udindo wa mtsogoleri wa Democratic Progress Party (DPP) ku konveshoni ikubwerayi, atuluka chipanichi.

Kabambe yemwe analinso gavanala wa Reserve Bank ya Malawi, walengeza za kutuluka kwake mchipani chotsutsa cha DPP kudzera mukalata yomwe atulutsa lero Lolemba pa July 15, 2024.

M’kalatayi iwo ati, “Nditaganizira mozama, ndaganiza zosiya kukhala membala wa chipani cha Democratic Progressive Party kuyambira pa July 14, 2024. Za nkhaniyi ndawadziwitsa kale a Prof. Arthur Peter Mutharika za ganizo langa.”

Iwo athokoza ndikufunira zabwino mtsogoleri wa chipani cha DPP a Mutharika komanso mamembala onse a chipanichi chifukwa chokhala nawo bwino pa nthawi yomwe anali mchipanichi.

Iwo ati ngakhale atuluka mchipani cha DPP akukhulupilirabe kuti mphamvu ndi kulimba mtima kwa Amalawi ndi zomwe zingapititse patsogolo dziko la Malawi ndipo ati dziko lino ndi lodzaza ndi kuthekera kochita bwino.

Ngakhale kuti mu kalatayi sanafotokoze za tsogolo lawo pa ndale, mphekesera zakhala zikumveka kuti a Kabambe akulowera ku chipani cha United Transformation Movement (UTM) komwe akufuna kukatenga udindo wa mtsogoleri wa chipanichi.

Advertisement

One Comment

Comments are closed.