Yemwe anali katakwe womwetsa zigoli mu timu ya mpira ya dziko lino Kinnah Phiri wauza Malawi24 kuti timu ya Flames ingakwanitse kupita ku AFCON pamaso pa Senegal komanso Burkina Faso, omwe ali mu Gulu L.
Kinnah Phiri akukhulupirira kuti timu ya Flames siili m’gulu lowopsa pangofunika kukonzekera bwino ndi kusankha wosewera abwino zikatero Flames akhoza kupita ku 2025 Morocco Africa Cup of Nations (AFCON).
Phiri, yemwe anaphuzitsapo timu ya Malawi ( Flames) adathandizira timuyi kuti ifike ku AFCON mchaka cha 2010, wati Dziko lino ikuyeneka kupeza njira zabwino zothandizira timuyi kumaliza patsogolo mugulu L.
M’gulu L Malawi ili pamodzi ndi Senegal, Burkina Faso, komanso Burundi, pamene ambiri sakuyipatsa mwayi timu ya Flames kumaliza pa mwamba kapena kukhala yachiwiri.
Phiri yemwe ndi katswiri wa zigoli 71 pamasewera 115, watinso Malawi inafika mu 2010 itathambitsa matimu akuluakulu monga.
“Tinakwanitsa kuyimitsa Egypt, komanso tinagonjetsa DRC ndi Guinea ndi kupitilira m’ndime yina, linali gulu lakufa.
Nthawi ino muli ndi Senegal, Burkina Faso, ndi Burundi, tili ndi mwayi woyenerera.
Tikungofunika kukonzekera bwino, kusankha bwino komanso kulimbikitsa osewera athu. Tili ndi mwayi waukulu wopambana ndipo ndizotheka,” adatero Phiri.