Thupi la Lucius Banda lifika m’dziko muno masanawa

Advertisement
Lucius Banda

Thupi la katswiri pa mayimbidwe, Lucius Banda, likuyembekezeka kufika m’dziko muno lero masanawa kuchokera m’dziko la South Africa komwe wamwalilira, ndipo pali chiyembekezo kuti lilowa m’manda Lachinayi sabata ino.

Izi ndi malingana ndi mwana wa malemu Banda, Benson yemwe wauza nyumba zina zowulutsira mawu m’dziko muno kuti thupi la malemu bambo ake lifika m’dziko muno kudzera pa bwalo la ndege la Chileka munzinda wa Blantyre.

Benson wati ndege yomwe inyamule thupi la malemu Banda ikuyembekezeka kutera pa bwalo la ndege la Chileka nthawi ya 2:30 masana a Lachiwiri, ndipo kenaka likatengeledwera kwawo ku Balaka.

Iye watinso Lachitatu kudzakhala mwambo wa mapemphero ndipo Lachinayi thupili lidzatengedwera pa bwalo la masewero la Balaka pomwe pakakhale mwambo wa misa omwe ukayendetsedwe ndi mpingo wa Katolika omwe malemuwa amapemphera.

Benson waonjezera kuti pali chiyembeko kuti thupi la bambo ake Banda omweso ankadziwika kwambiri ndi dzina loti “Soja”, lidzalowa m’manda Lachinayilo ukadzatha mwambo wa mapemphero pa bwalo la masewero la Balaka.

Lucius Banda yemwe anabadwira m’mudzi mwa Sosola, mfumu yaikulu Nsamala, m’boma la Balaka, wamwalira Lamulungu pa 30 June 2024 pomwe amalandira thandizo la mankhwala pa chipatala china m’dziko la South Africa.

Advertisement