Thupi la Mr Ibu lalowa m’manda

Advertisement
Mr Ibu

Patadutsa pafupifupi miyezi inayi (4) chimwalilireni, thupi la katswiri pa nkhani ya zisudzo m’dziko la Nigeria a John Okafor omwe amadziwika kwambiri ndi dzina loti Mr Ibu, layikidwa m’manda tsopano.

Thupi la Mr Ibu omwe adamwalira pa 2 March chaka chino atadwala kwa nthawi yayitali, layikidwa m’manda Lachisanu pa June 28, 2024, kwawo kwa Eziokwe Amuri, Nkanu West. Local Government Area, Enugu State m’dziko la Nigeria.

Mwambo woyika thupi lawo m’manda omwe unali wa pa mwamba komanso opeleka chidwi kwambiri, wachitika pomwe panangotsala masiku anayi okha kuti pathe miyezi inayi (4) chimwalilireni.

Pofotokoza za kuchedwa kuyika thupili m’manda, mchimwene wa Mr Ibu, Sunday Okafor, posachedwapa adawuza nyumba zina zosindikiza nkhani m’dziko la Nigeria kuti akubanja amafuna kuti katswiri pa zisudzoyu adzapatsidwe ulemu molingana ndi momwe analili ali moyo.

Poyankhula pa mwambo wa malirowa, Sunday wati akubanja ndiwosangalala kuti m’bale wawo wasiya cholowa chabwino chomwe ndi chikondi, kuseka komanso moyo okhala bwino ndi anthu ena.

Pamalirowo panafika achibale, abwenzi, komanso akatswiri osiyanasiyana omwe ena mwa iwo adachita zisudzo ndi malemu Mr Ibu. Ngakhale unali mwambo womvetsa chisoni, anthu ambiri anasangalalira malemu Mr Ibu kamba ka zisudzo zomwe ambiri ati zinabweretsa chisangalalo pamiyoyo yawo.

Malemu John Okafor anabadwa pa 17 October 1961 ndipo mkazi yemwe amusiya pano Stella Maris Okafor, anali naye ana atatu. kupatula apo iwo asiya ana enaso kuchokera kwa mkazi yemwe anasiyana naye banja mbuyomu.

Iwo adachita nawo mafilimu opitilira 200 a Nollywood kuphatikiza; Mr Ibu (2004), Mr Ibu 2 (2005), Police Recruit (2003), Bafana Bafana (2007), 9 Wives (2005), ndi ena ambiri.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.