Chakwera akanika kutsata lamulo, sanasankhebe wachiwiri wake

Advertisement
President Lazarus Chakwera

Mtsogoleri wa dziko la Malawi, Lazarus Chakwera, wakanika kutsatira malamulo pamene mpaka pano sanasakhebe wachiwiri wake.

Kutsatira imfa ya wakale wachiwiri kwa pulezidenti Dr. Saulos Chilima yemwe analowa mmanda pa 17 June, Bungwe loyendetsa malamulo m’dziko muno linauza Chakwera kuti akuyeneka kusakha omutsatira watsopano pasanapitilire pa 19 June. 

Anthu ambiri m’dziko muno dzulo, tsiku loyikikali, anakhala ndi chidwi ndipo anaswera pa makina a intaneti kutsatira nkhani koma kunali chete ochokera kwa a Chakwera. 

Mtolankani wa Malawi24 ku Mzimba, usiku wapitawu, anayendera malo wosiyana siyana monga madera a Chimkusa, Engalaweni, Kazomba , kwa Gama ndi malo ena ndipo anapeza anthu ali ndi chidwi kumvera wayilesi ndi nkhani pa matsamba amchezo kuti amve za kusakhidwa kwa yemwe akhale wachiwiri wa mtsogoleri wa dziko lino.

Masiku ochepa apitawa, nduna yofalitsa nkhani a Moses Kunkuyu inatsimikizira mtundu wa Malawi kuti Pulezidenti wadziko lino alemekeza malamulo.

“Pulezidenti Chakwera ndi mtsogoleri wolemekeza malamulo ndipo ndi nenetse pano kuti asankha wachiwiri wawo munthawi yoyikika” anatero a Kunkuyu pa mtsonkhano ndi wolemba nkhani.

Pakadali pano ambiri akukambirana maina wosiyanasiyana womwe iwo akuona kuti mwina atha kusankhidwa kukhala wachiwiri kwa Chakwera.

Advertisement