Talandira mayankho opatsa chilimbikitso pa nkhani ya kafukufuku – Kunkuyu

Advertisement
Moses Kunkuyu

Nduna yofalitsa nkhani a Moses Kunkuyu ati boma lalandira mayankho opatsa chilimbikitso pa nkhani ya kafukufuku wa ngozi yomwe inakhudza wachiwiri wa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima ndi ena asanu ndi atatu.

Poyankhura pa msonkhano wa atolankhani lero ku Lilongwe, a Kunkuyu ati zinthu zambiri zokhudza tsatane tsatane wa kafukufuku yemwe akuyembekerezedwayu afotokozerabe a Malawi. 

Pankhani yokhudza chuma chomwe chinagwiritsidwa ntchito pa mwambo wa maliro, ndunayi yati ikudikira lipoti kuchokera ku komiti yomwe inasankhidwa kuti iyendetse malirowa.

“Komiti yomwe inasankhidwa kuti iyendetse mwambo wa a bale athu onse asanu ndi anayi inapatsidwa ndalama zoti chilichonse chiyende bwino. Panaperekedwa ndalama n’cholinga choti a chipani chomwe malemu a Chilima anali mtsogoleri cha United Transformation Movement (UTM) kuti abweretse owatsatira awo komanso chakudya chikhale chokwanira,” anatero pofotokoza.

A Kunkuyu ati pa nkhani yoyika chikumbutso pamalo pomwe panachitira ngozi, boma libweretsabe yankho lake chifukwa pamayenera pakhale dongosolo. 

Iwo achenjeza omwe amafalitsa mauthenga osiyana ndi zomwe boma limafotokozera ku mtundu wa a Malawi pa nthawi yomwe kunachita ngozi kuti ma umboni onse alipo komanso ena omwe anayambitsa chisokonezo ku Ntcheu ati ali m’manja mwa polisi.

Ndunayi ya thokozanso anthu a dziko lino posunga bata komanso powonetsa umodzi pa nthawi ya chisoniyi zomwe zawonetsa kuti mu umodzi muli mphamvu ngakhale ena amafuna kudanitsa komanso kugawanitsa anthu.

Dziko la Malawi linataya wachiwiri wa mtsogoleri wake komanso Shanil Dzimbiri (Balaka) ,Chisomo Chimaneni (Ntchisi), Dan Kanyemba (Lilongwe), Colonel Owen Sambalopa (Zomba), Major Wales Aidin (Mangochi), Flora Selemani Ngwirinji (Thyolo) and Lukas Kapheni (Kasungu) pa ngozi ya ndege lolemba sabata yatha yomwe inachitika mu nkhalango ya Chikangawa m’boma la Mzimba.

Advertisement