Thupi la mayi Dzimbiri lanyamuka  lero kupita ku Balaka

Advertisement
Patricia Shanil Dzimbiri

Thupi la yemwe adakhalapo mkazi wa pulezidenti wakale a Bakili Muluzi, mayi Patricia Shanil Dzimbiri, tsopano  lanyamuka kupita kwawo ku mudzi kwawo ku Balaka komwe likaikidwe m’manda lachisanu.

A Dzimbiri, komanso wachiwiri wakale wa mtsogoleri wa dziko lino, a Saulos Chilima ndi  ena asanu ndi awiri anamwalira pa ngozi ya Ndege yomwe idachitika Lolemba mu nkhalango ya Chikangawa m’boma la Mzimba.

Nduna ya maboma ang’onoang’ono a Richard Chimwendo Banda ati ndiwokhudzika kwambiri ngati munthu komanso boma chifukwa dziko lataya munthu yemwe amaonetsa chidwi pa nkhani za ndale komanso olimbikira pa ntchito yawo.

A Chimwendo analimbikitsa akubanja kwa malemuwa kuti akhale olimba ntima komanso kupemphera pamene iwo angakhalenso dziko, likudutsa nyengo imeneyi.

Oyimira kuchipani chotsutsa cha Democratic Progressive ku nyumba ya malamuro, a George Chaponda, ati anali ndi chikhulupiriro kuti wachiwiri wa mtsogoleri komanso ena asanu ndi atatu omwe anali mundegeyi apulumuka pangoziyi komano pano ndi wosweka mtima komanso othodwa ndi imfa imeneyi.

“Ndikusowa chonena taluza anthu olimbikira kwambiri. Akubanja kwa mayi Dzimbiri tili nawo limodzi. Tikanena mbiri ya a Chilima anayamba ndale pamene analowa chipani cha DPP ngati otsatira wa mtsogoleri wakale wa dziko lino a Professor Author Peter Mutharika. Tagwiranawo bwino ntchito ndipo anali munthu olimbikira kwambiri pano kwathu ndikulira kuti dziko lino lataya munthu yemwe anali opaturika pa zinthu zambiri,” iwo anafotokoza.

Ena mwa anthu omwe amwalira pa ngoziyi ndi Chisomo Chimaneni wochokera ku Ntchisi , Dan Kanyemba (Lilongwe), Colonel Owen Sambalopa (Zomba), Major Wales Aidin (Mangochi), Flora Selemani Ngwirinji (Thyolo) and Lukas Kapheni (Kasungu).

Advertisement