Mayi akwatirana ndi mwana wake omubereka 

Advertisement
Zimbabwe

Mzimayi wina wa zaka 40 zakubadwa  yemwe ndi mzika ya dziko la Zimbabwe watutumutsa anthu dzikolo atalengeza  kuti ali ndi pakati ndipo  bambo ake ndi mwana wake omubala wa zaka 23 zakubadwa.

Betty Mbereko wa zaka 40 zakubadwa amakhala ndi mwana wake wa mwamuna, Farai Mbekero kamba koti bambo ake a Farai anamwalira zaka 12 zapitazo ndipo mayiwa ndi amene aphunzitsa mwana wawo  sukulu Kufikira wamaliza ndi kupeza ntchito.

Mayiyu  wati ndi okhutira kukwatirana  ndi mwana wake ndipo mimba yomwe ali nayo ya  miyezi 6 ndi ya mwanayo, pa chifukwa ichi sakufuna kuti akwatirane ndi mphwawo wa mwamuna wake.

Awiriwa anawaitanitsa ku bwalo la mfumu koma mayiyu anamenyetsa khwangwa pa mwala kuti sangasinthe chiganizochi kamba koti mwana wawo anavutikira kumulipirira  sukulu fizi kufikira wamaliza ndi kupeza ntchito ndipo ati nthawi yakwana  tsopano kuti adye ntukuta lawo.

Farai wati ali okonzeka kukwatirana ndi mai ake ndipo alipira ndalama imene bambo ake anarephera kumalizitsa lobola la mai ake.

Iye anapitiriza kunena kuti palibe chifukwa chobisa pa zimene akuchita ndi mai ake ndipo mimbayo wayivomereza kuti ndi yake maso muli gwa.

Mfumu Nathan Muputirwa ya m’dera limene Betty amakhala yadandaula ndi mchitidwewu kamba koti ndi zosemphana ndi chikhalidwe cha muno mu Africa.

Malo mwake mfumuyi yathamangitsa awiriwa m’dera lake ndipo Farai ndi mai ake asamuka m’derali koma kumene apita sikudziwika.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.