SULOM ilanga omwe anagenda pa bwalo la Kamuzu

Advertisement
Bullets

Bungwe la Super League of Malawi (SULOM) ladzudzula zipolowe zomwe zinachitika Lamulungu pa masewero a pakati pa FCB Nyasa Big Bullets komaso Silver Strikers munzinda wa Blantyre ndipo yati ilanga onse omwe apezeka olakwa.

Anthu okwiya omwe akuganizilidwa kuti ndi ochemelera timu ya Bullets anayamba kugenda m’bwalo la masewero potsatira chigoli chomwe anachinya Chisisi Maonga pa mphindi ya 90 ya masewerowa omwe anachitikira pa bwalo la Kamuzu. 

Anthuwa anachita izi kamba ka mkwiyo ponena kuti chigolichi chinali cha ofusayidi (offside) ndipo ataona momwe miyala imavumbira, oyimbira Gift Chicco anayimitsa kaye masewerowa kwa mphindi zingapo.

FCB Nyasa Big Bullets vs Silver Strikers
SULOM yati ilanga omwe achita izi.

Kudzera mu kalata yomwe latulutsa potsatira zomwe zachitikazi, bungwe la SULOM lati mchitidwewu ndi osaloledwa m’masewero a mpira wa miyendo ndipo lati lipeleka chilango choyenera kwaonse omwe apezeke olakwa.

“SULOM ikudzudzula mwamphamvu ziwawa zomwe zachitika lero pamasewera a FCB Nyasa Big Bullets ndi Silver Strikers pa Kamuzu Stadium mumzinda wa Blantyre. Kugenda miyala komwe kunachitika ndikosavomerezeka ndipo kumasemphana ndi mzimu wamasewera komanso zikhalidwe zomwe timatsatira mu ligi.

“Tikutsimikizira onse okhudzidwa kuphatikizapo osewera, ochemelera ndi akuluakulu kuti Super League of Malawi silola khalidwe ngati limeneli. Chilango choyenera chidzaperekedwa kwa omwe achita izi motsatira malamulo omwe akugwiritsidwa ntchito,” yatelo SULOM.

Bungweli lati ndilodzipereka kuonetsetsa kuti chitetezo kwa onse omwe akutenga nawo gawo pamasewera ali onse mu ligi ndichokhwima ndipo yati igwira ntchito limodzi ndi magulu opeleka chitetezo kuti afufuze bwino za nkhaniyi.

Pakutha pa masewerowa “Ma Bankers” apambana ndi chigoli chimodzi kwa duu ndipo tsopano ili ndi ma poyitsi 25 motsatizana ndi Kamuzu Barracks yomwe ili ndi mapoyitsi 18. Aka ndikoyamba kuti Silver ipambane “Maule” m’masewero a ligi pa zaka 8. 

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.