Bangwe All Stars ayionetsa Bangwe molapitsa

Advertisement

Bangwe All Stars yagonja ndi Premier Bet Dedza Dynamos ndizigoli zitatu kwa duu pabwalo lamasewero la Dedza lero mu TNM Super League.

Dedza Dynamos inapeza chigoli chake choyamba kudzera mwa Lughano Kayira  pamphindi makumi awiri ndi zinayi.

Mchigawo choyamba chomwecho Pamphindi makumi anayi ndi imodzi naye Chifuniro Mpinganjira anakankhira chikopa pagolo kupangitsa Dedza Dynamos kutsogola ndi zigoli ziwiri.

Dedza Dynamos inapezanso chigoli chachitatu kudzera mwa Chifuniro Mpinganjira kupangitsa Dedza Dynamos kupeza zigoli zitatu kwa duu.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.