Kamuzu Barracks yaswa timu ya Mighty Tigers 

Advertisement
Kamuzu Barracks

Kamuzu Barracks yapambana pamasewero omwe analiko lero mu TNM Super League pomwe imasewera ndi anyamata a Mighty Tigers ndi zigoli zitatu kwa ziwiri.

Pa masewero omwe anachitikila pa Kamuzu Stadium, Kamuzu Barracks inapeza chigoli choyamba pa mphindi khumi komanso chigoli chachiwiri pamphindi makumi awili ndi anayi ndipo zonse anagoletsa ndi Zeliati Nkhoma.

Kamuzu Barracks sinasiyire pompo koma kuthiranso chigoli china cha nambala 3 mchigawo chachiwiri chomwe anagoletsa Ndaona Daisi, kupangitsa Kamuzu Barracks kutsogola ndi zigoli zitatu.

Zinthu zinatembenuka mchigawo chachiwiri chomwecho pomwe Mighty Tigers inavumbitsa zigoli mowilikiza kugolo la Kamuzu Barracks zomwe zapangitse kuti masewero athere zigoli zitatu kwa ziwiri.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.