A Mutharika Sayima 2025 mumve ine – Msonda

Advertisement
Ken Msonda - Richard Chimwendo Banda - Dowa Rally

M’modzi mwa omwe analowa chipani cha Malawi Congress (MCP) kuchoka ku chipani cha Democratic Progressive (DPP) a Ken Msonda ati  mtsogoleri wa chipani cha DPP a Peter Mutharika sadzaima nawo pa masankho a chaka cha mawa ngakhale  ananena ku Mjamba kuti ayima.

A Msonda alankhula pa nsonkhano wa ndale wa chipani cha MCP lamulungu ku Dowa, ndipo ati anthu akuyenera amve zimene a Msonda akunena chifukwa akuwadziwa a Mutharika m’mene alili.

A Msonda omwe anachotsedwa ku DPP kamba kosatsata mwambo ku chipanicho ati a Chakwera asatekeseke ndi a Mutharika.

Ken Msonda Dowa Rally
A Mutharika sadzaima nawo pa masankho a chaka cha mawa – Msonda.

“Mumve ine, a Mutharika chaka cha mawa sayima nawo pa chisankho ndikudziwa ndine za akulu aja, akulu aja sayima, amene amadziwa matenda ndi amene akudwazika ine ndinaadwazika,” anatero polankhula a Msonda.

Iwo anatsindikanso kuti ku DPP anawachotsa chifukwa cha chilungamo pamene amawuza otsatila chipanicho kuti adzitha kuyamika zomwe a Chakwera akuchita pakadali pano koma ambiri anawada chifukwa  cha mfundoyi ndipo anati ambiri ku DPP ndi asanibalati anthu osayamika. 

M’mawu awo a Richard Chimwendo Banda nduna ya za maboma ang’ono anati a Mutharika ngakhale atayima koma sangapambane pa masankho a chaka chamawa.

Pa msonkhano womwe anachititsa ku Mjamba mu mzinda wa Blantyre  mtsogoleri wa chipani cha DPP a Peter Mutharika anatsindika ku mtundu wa  aMalawi kuti chaka chamawa adzapezeka nawo pa tsamba la anthu amene adzapikisane nawo pa mpando wa mtsogoleri wa dziko ndipo iwo anati adzapambana ndipo adzabwezeretsa dziko mchimake  mu mzaka ziwiri zokha.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.