Achinyamata khumi ndi awiri omwe anayiwala kuti ukayendera n’zengo usati asakhwi afumbura, awathamangitsa m’dziko la Israel kamba kotaya chingamu chifukwa cha mtedza olawa.
Sabata latha, a Polisi m’dzikolo anamanga achinyamata okwana makumi anayi ndi mphambu zisanu chifukwa chothawa ntchito zosiyanasiyana zomwe anapitira m’dzikolo ndikupita kukayamba ntchito ku kampani zina m’dziko momwemo.
Mwachiwerengerochi, khumi ndi awiri anali achinyamata ochokera m’dziko muno omwe akuti anasiya ntchito ya kumunda yomwe anapitira m’dzikolo ndikukayamba kugwira ntchito ku kampani yopanga bisiketi.
Potsatira izi, boma la Israel lalamura kuti anyamata onse omwe akukhudzidwa ndi nkhaniyi abwelere m’mayiko akwawo kaamba kophwanya pangano la mgwirizano wa ntchito zomwe anapitira m’dzikolo.
Boma la Malawi, kudzera mu kalata yomwe wasainira ndi nduna yowona zofalitsa nkhani, a Moses Kunkuyu, latsimikiza za kuthamangitsidwa kwa achinyamatawa ndipo lati achinyamata okwana anayi afika kale m’dziko muno Lachiwiri pa 7 May, 2024.
Malingana ndi kalatayi, achinyamata ena asanu ndi atatu (8) omwe anakhudzidwa ndi nkhaniyi, akuyembekezekanso kubwelera kuno ku mudzi lero Lachitatu pa 8 May, 2024 kudzera pa bwalo la ndege la Kamuzu munzinda wa Lilongwe.
Pakadali pano dziko, la Malawi lalangiza achinyamata onse omwe akugwira ntchito m’dziko la Israel kuti ayesetse kutsata malamulo a m’dzikolo ndikusunga mwambo ndicholinga chofuna kupewa nkhani zochititsa manyazi ngati izi.
Boma la Malawi lati kupatula kuchititsa manyazi dziko lino, nkhani za mtunduwu zili ndikuthekera kolepheretsa a Malawi ena akupeza mwayi wa ntchito m’dziko la Israel komaso mayiko ena.