Nduna yakale ya za masewero mu ulamuliro wachipani cha UDF yamwalira

Advertisement

Nduna yakale ya za masewero mu ulamuliro wachipani cha United Democratic Front (UDF) a Moses Dossi yamwalira.

Mwana wamalemuwa Susan wati a Dossi amwalira kuchipatala cha Blantyre Adventist kucha kwa Lachinayi ali ndi zaka 70 ndipo wati adzawakumbikira bambo wake chifukwa adali munthu okonda mtendere komanso okonda aliyense.

A Dossi, omwenso adakhalapo phungu wakunyumba yamalamulo mdera la Chikwawa West, adatchukapo zaka zambuyomu chifukwa cha luso lawo lowunikira bwino momwe masewero ampira akuyendera ndipo amadziwika ndi dzina loti “Man on the touch line.”

Malemuwa ayikidwa m’manda Loweruka ku mudzi kwawo kwa Chapananga m’boma la Chikwawa ndipo thupi lawo litengedwa ku nyumba ya chisoni ya Mthuzi lero masana pomwe lipite ku Manja kwa mwana wawo Moses komwe anthu akhale akukhudza malirowa.

A Dossi asiya mkazi ndi ana asanu ndi m’modzi.

Thupili linyamulidwa Lachisanu kupita ku mudzi kwawo.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.