A Polisi Boma la Machinga alimbikitsa chitetezo m’malire a Malawi ndi Mozambique

Advertisement

A polisi m’boma la Machinga alimbikitsa chitetezo pakati pamalire a dziko la Malawi ndi Mozambique pomwe akhazikitsa makomiti owona zachitetezo chakumadera akumidzi.

A Polisiwa alangizanso mzika za dziko lino kuti zidzikhala tcheru pankhani za umbanda ndi umbava komanso adzikanena ku polisi ngati akuwona anthu okayikitsa mdera lawo.

Mkulu woona zachitetedzo chakumadera akumidzi pa polisi ya Machinga, Sub Inspector Masautso Katemera ndiyemwe wayankhula izi m’madera a mfumu yaikulu Mtumbwinda ndi Sub T/A Adamson.

A Katemera ati kudera ngati kukuchitika za umbanda ndi umbava, chitukuko sichimapita patsogolo popeza anthu amalephera kupanga chitukuko powopa akuba ndipo ati nkoyenera kuti makomiti achitetezowa adzigwira ntchito yopereka chitetezo masana ndi usiku.

Iye adalangizanso makomitiwo kuti adzigwira ntchito yawo mokhulupirika popewa zachinyengo zilizonse ndipo adaonjezera popereka chenjezo kuti membala aliyense opezeka akuchita za umbanda kapena zachinyengo adzayimbidwa mulandu.

Pamenepa, a Katemera adapemphanso anthu a m’madera awiriwa Adamson kuti adziwonetsetsa kuti anthu sakuzembetsa mbeu monga chimanga ndi fodya kumakagulitsa m’dziko la Mozambique.

“Tiyeni tigwirane manja polimbikitsa chitetezo madera mwathu popeza umbanda ndi umbava umabwedzeretsa chitukuko mbuyo ndipo inu amene mwasankhidwa kuti mudzipereka chitetezo m’madera akuno, muwonetsetse kuti anthu akukhala mwamtendere,” anatero Katemera.

Poyankhulanso pamkumanowo Mfumu yaikulu Mtumbwinda inathokoza a Polisi a Boma la Machinga chifukwa chobwera kudzakhadzikitsa makomiti owona zachitetezowa m’dera lawo ndipo adati izi zipangitsa kuti chitetezo chikhale champhamvu.

Iwo adalimbikitsa makomiti achitetedzowo kuti adzigwira limodzi ntchito ndi apolisi poyendera masana ndi usiku kupereka chitetedzo kuti anthu asamakhale ndimantha.

Advertisement