Palibe kuthawa apa – a bwalo ampanilira Batatawala

Advertisement
Aslam Abdul Karim Batatawala Appears in Court on Corruption Charges

Amafuna kutulukira pawindo koma abwalo akamumbwandira. Mulandu wake wa katangale upitilira basi, ndipo akapezeka olakwa Batatawala n’kutheka akasewenza jele.

Oganiziridwa pa milandu ingapo ya katangale, a Abdul Karim Batatawala achoka ndi nkhope ya manyazi ku bwalo la milandu dzulo pamene a bwalo alamula kuti mulandu wawo umodzi pa ingapo okhudza katangale upitilirebe.

A Batatawala amene akuganiziridwa kuti adachita za katangale, anapempha kuti bwalo lithetse mlandu ngakhale kuti sunamalizidwe kumvedwa ati chifukwa a bungwe lothana ndi katangale la ACB akuwayimba milandu yosayenelera.

Mwa zina, a Batatawala kudzera mwa owayimira milandu amati a bungwe la ACB akuwayimba milandu yosagwirizana ndi zimene akuti iwo anachita. Koma pounikirapo a bwalo ati zimene amadandaula mkulu oganiziridwa kuchita zoipayu zinali zosamveka kwenikweni. A bwalo ati bungwe la ACB lidawatchaja iwo ndi milandu yoyenera.

Dandaulo la Batatawala lidabwera ngakhale kuti bungwe la ACB linayamba kale kubweretsa poyera umboni wa zakuipa zomwe mkulu wa malondayu adachita. Bungweli ndi kuti tsopano lidangotsala ndi mboni ziwiri kuti likwangule.

Anthu ena adaona ngati zimene amadandaula mkuluyu kunali chabe kuzemba chigamulo chifukwa adaona kuti madzi achita katondo mu bwalo.

Mwa zina, a Batatawala akuyimbidwa mulandu owonjezera mitengo pa katundu amene anagulitsa ku nthambi ya boma yoona ndi kulowa m’dziko muno ya Immigration. Malinga ndi bungwe la ACB, a Batatawala adagwirizana ndi a Elvis Thodi amene adali mkulu wa nthambiyi kuti asupule dziko la Malawi ndalama za nkhani nkhani.

Zina mwa ndalama zidasupulidwazi zidali ndi kuthekera kothandiza pa chitukuko cha dziko koma ati zidapita mmatumba mwa akulu awiriwa.

A Batatawala amene adachita ziii pakati apa boma litalamula kuti asamachitenso nawo malonda ayambilanso kumveka sabata lino atalamula apolisi kuti anjate mtolankhani wina, Macmillan Mhone, kamba koti adalemba nkhani zina zoulula kuti iwo adakachitabe za machawi ndi boma la Malawi. A Polisi adati iwo adamanga a Mhone poulutsa nkhani zomwe zingathe kudzetsa chisokonezo komanso kuti ati amafuna kubera Batatawala.

Koma nyumba ina yolemba Mawu yati uwo udali upo chabe ochoka kwa Batatawala amene adawatchulanso kuti ndi a mzawo a Chakwera.

Advertisement