Bambo wina wa zaka 32 ku Blantyre, ali muululu owopsya pa chipatala cha Queen Elizabeth munzinda wa Blantyre pomwe wavulazidwa ndi nyesi za magetsi pomwe akuganizilidwa kuti amafuna kuba mawaya a magetsi.
Malingana ndiwofalitsa nkhani pa polisi ya Limbe, Sergeant Aubrey Singanyama, bambo oganizilidwa kubayu wazindikilidwa ngati a Dickson Khoviwa omwe akuti akumana ndi zakudazi Lachitatu pa 10 April pa Maselema, mphepete mwa nsewu wa Masauko Chipembere.
A Singanyama ati cha m’ma 3 koloko m’bandakucha wa tsikuli, Khoviwa pamodzi ndi mzake wina yemwe akuzindikilidwa ngati Mafo, wochokera ku Bangwe, anapita pa Maselema ndicholinga chofuna kukaba mawaya a magetsi.
Atafika pa malowa, mwa mtima bii, awiriwa anayamba kukumba pansi ndicholinga choti achotse mawaya a magetsi omwe anali atalumikizidwa ku pholo lina la magetsi.
Koma poti tsiku la 40 likakwana silimazembeka, awiriwa ali nkati mokumba mawayawa, Khoviwa anagwidwa nyesi ya magetsi yomwe inamuvulaza kwambiri ndipo pomwepo anagwa pansi chifukwa cha ululu.
Mafo ataona kuti mzakeyo wavulala kwambiri, anangoti phanzi thandizo, ndipo analiutsa liwiro la mtondo wadooka, kuthawa, kumusiya nzakeyo akubuula ndi ululu wa mabala akewo.
Anthu ena omwe anapeza mkuluyu ali thapsya ndi omwe anakanena za nkhaniyi ku polisi ya Limbe ndipo apolisi anathamangira pa malowa kuti akaone kuti zakhala bwanji.
Apolisi atafika pa malopa ndi pomwe zinadziwika kuti mawaya omwe Khoviwa ndi nzake Mafo amakumba, anali olumikizidwa ku mapholo omwe amanyamula magetsi a mphamvu yochuluka kwambiri.
Apa apolisiwa sanamve chisoni ndipo ngakhale Khoviwa anali muululu, anamuthira dzingwe kenaka ndikupita naye ku chipatala cha Queen Elizabeth komwe akulandirabe thandizo la mankhwala mpaka pano.
Pakadali pano, Sergeant Singanyama wati apolisi ya Limbe akhazikitsa kafukufuku ofuna kugwira Mafo yemwe pano sakudziwika komwe ali.
Dickson Khoviwa amachokera m’mudzi wa Nasawa mfumu yaikulu Kuntumanji m’boma la Zomba.