Apolisi anjata mayi kamba kotentha ndikuvulaza mwana wake

Advertisement
Machinga

A polisi m’boma la Dowa akusunga mchitolokosi a Chimwemwe Kayera azaka 35 zakubadwa, kamba kowaganizira kuti anawotcha ndi kuvulaza mwana wawo wamamuna wa zaka khumi ndi ziwiri (12).

Mneneri wa Polisi ya Dowa a Seageant Alice Sitima auza Malawi24 kuti nkhaniyi inachitika Lachinayi pa 4 April 2024 nthawi ya 7 kaloko madzulo mmudzi mwa Chiwoza m’dera la mfumu yayikulu Msakambewa.

A Sitima ati patsikuli, bambo Bikinao Nkhoma ndi akazi awo a Chimwemwe Kayera anapita kumunda ndipo mwanayu atadzuka anaganiza zophika mbatata kuti adye ngati chakudya cha kadzutsa.

Pamenepo woganizilidwawa atafika kuchoka kumunda adapeza mwanayu ataphika mbatata popanda chilolezo kuchokera kwayiwo ndipo izi zinapangitsa kuti mayiyu amuthire mwanayu mbatata zamoto.

Pamenepo a Nkhoma anapeza mwana wawoyu akulira ndipo ali muululu woopsya zomwe zinapangitsa kuti amutengere kuchipatala chachikulu cha Dowa komwe akulandira thandizo lamankhwala.

Atapanga kafukufuku wawo, a polisi anakawanjata mayiwa pamene anakabisala kumudzi kwawo ndipo akuyembekezera kukaonekera ku bwalo la milandu kuti akayankhe mulandu wovulaza mwana wawo.

Advertisement