DPP sidzabweleranso m’boma ndipo 2025 Chakwera awina ndi 70% – Chimwendo

Advertisement

Fikitsani uthengawu ku Mangochi kwa a Mutharika: zobwelera m’boma ndi maloto chabe, a Malawi onse maso nga! pa Chakwera, watero ndi nduna ya Maboma Aang’ono a Richard Chimwendo Banda.

Polankhula potsekera zokambirana mu nyumba ya malamulo lero, a Chimwendo Banda ati chipani chotsutsa cha DPP chinatuluka m’boma ndipo sichibweleranso. Iwo ati a Malawi ambiri akukumbukirabe mavuto amene anawaona ndi chipanichi.

“Kaya Kamba atadikhula, sizingatheke kuti DPP ibwelerenso,” kutanthauzira kwa mawu awo kutha kukhala kotero.

Mawu a Chimwendo adza pomwe a Peter Mutharika dzulo lomweli anabwereza kunena kuti DPP ibwelerenso m’boma ndipo mtsogoleri wake akhala iwo basi. Koma a Chimwendo ati olo DPP itabwera ndi mnyamata kaya ndi gogo, sikulowanso m’boma.

“A Malawi chikhulipiliro chawo chili mwa a Chakwera ndipo pa chisankho cha chaka chamawa azawina ndi 70% ya mavoti,” iwo anatero.

Mukuona kwawo a Chimwendo, palibenso cholepheretsa a Chakwera kupitiriza kutsogolera dziko lino ndipo olo za masankho a chibwereza sizizafunika.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.