Pawiri pawiri sipauzilika: apolisi ati wapolisi nzawo yemwe wapha bwezi lake m’mawa wa Lachitatu kenaka naye ndikudziphaso, anali pa banja ndi nkazi wina yemwe anabelekerana naye ana awiri.
Wanena izi ndi ofalitsa nkhani za a polisi m’dziko muno a Peter Kalaya omwe azindikira wa polisi yemwe wadziphayu ngati Sergeant Paul Mpheluka yemwe wapha Sabina Bwanali.
A Kalaya ati a Mpheluka anali okwatira komaso asiya ana awiri ndipo kupatula apo analiso paubwenzi wa nseri ndi Sabina .
Ofalitsa nkhani za polisiyu wati usiku wa Lachiwiri pa 2 April, 2024, a Mpheluka ndi Sabina anali pa malo ena omwera chakumwa cha ukali ndipo akuti macheza ali mkati awiriwa anasemphana chichewa.
Apolisi ati kusemphanaku kunabwera kamba koti pa nthawiyo Sabina amafuna amusiye Mpheluka kuti akatengane ndi mamuna wina kukasangalala mwa chilengwedwe zomwe akuti zinakwiyitsa mphongoyi.
Kutacha Lachitatu m’mawa, Mpheluka anapita ku ntchito kwake monga mwa nthawi zonse ndipo anakatenga mfuti ponama kuti akukapereka chitetezo Ku kampani ina m’boma lomweli la Dedza.
Atatenga mfutiyi, Mpheluka anauyatsa ulendo kulunjika ku nyumba kwa bwenzi lake la nseli Sabina komwe anamupeza ali mnyumba mwake ndipo atamutsekulira, naye analowa mnyumba momwemo.
Anakadziwa Sabina sanakatsekura chitseko kamba koti Mpheluka atalowa anamuombera bwenzi lakeyo kenaka nkudziomberaso yekha ndipo anthu oyandikana ndi nyumbayo atadabwa ndi kulira kwa mfuti, anathamangira kukanena ku polisi.
Apolisi anathamangira ku nyumbayi koma momwe amafika, anakapeza awiriwa atafa kale ndipo akuti pambali pa matupi awo panali mfuti, zipolopolo ziwiri zogwiritsa kale ntchito ndi zipolopolo zitatu zosagwiritsa ntchito.