Nthambi yowona za nyengo ndi kusintha kwa nyengo ya Department of Climate Change and Meteorological Services (DCCMS), yati madera ena mdziko muno alandira mvula yopyoola muyeso mwezi uno ndipo pali chiopsezo cha madzi osefukira m’madera ena mchigawo cha ku mpoto.
Izi ndi malingana ndi mauthenga a za nyengo omwe nthambiyi yatulutsa Lachiwiri pa 2 April, 2024 omwe akusonyeza kuti madera ena mdziko muno apitilira kulandira mvula mwezi uno wa April.
Nthambi ya DCCMS yati pali chiyembekezo choti maboma ena mchigawo cha ku mpoto omwe ndikuphatikizapo Karonga komaso Nkhatabay komaso ena amchigawo chapakati, alandira mvula yapakati kapena yochulukirapo.
“Tiyembekezere nyengo ya mvula ya mlingo wapakati kati kapena kuposerapo m’madera akumpoto ndi ena am’chigawo chapakati pomwe kumwera kukhala kwa mlingo wapakatikati kapena kucheperako.
“Ngakhale zili chonchi, mlingo omwe ukuyembekezereka m’madera ambiri suposa 20mm ndipo kwina siigwa kumene. Pomwe m’madera ambiri akumpoto akuyembekezereka kukhala ndi mlingo wa pakati pa 100-350mm,” yatelo nthambi ya za nyengo.
Nthambiyi yatiso madera angapo makamaka mchigawo cha kumpoto, ali pachiopsezo cholandira madzi osefukira ndipo yalangiza anthu m’madera amenewo kukhala tcheru kwambiri.
“Langizo: Chiopsezo chakusefukira kwa madzi ndichokwerabe ku Karonga ndi ku Nkhatabay. Choncho, tikhale atcheru ndi osamala kuopa kutaya miyoyo ndi katundu,” wateloso uthenga wina kuchokera ku nthambi ya DCCMS.
Ngakhale zili choncho, DCCMS yati nyengo yamvula ya 2023/2024 ikuyembekezereka kuyamba kupita kumapeto ndipo yati nyengoyi ikuyembekezereka kutha msanga m’madera ambiri akumpoto pomwe madera ena akumwera ndi pakati ikhoza kudzatha mochedwerapo pang’ono poyerekeza ndi mene zimakhalira mbuyomu.