Apolisi apha mbava poyiwombera

Advertisement
Malawi 24 news logo

Apolisi ku Ndirande mu mzinda wa Blantyre, awombera ndikupha mzibambo wina yemwe akumuganizira kuti amafuna kukaba ku nyumba kwa wachiwiri kwa wamkulu wa apolisi m’chigawo cha ku m’mwera cha ku mzambwe.

Malingana ndi ofalitsa nkhani za apolisi m’chigawo cha ku m’mwera cha ku mzambwe, a Joseph Sauka, tsizinamtoleyu wakumana ndi mazangazimewa usiku wa Lolemba pa 1 April, 2024.

A Sauka ati patsikuli, munthuyu komaso nzake wina yemwe anathawa ndipo pano sakudziwika komwe ali, anapita ku nyumba ya wachiwiri kwa wamkulu wa apolisi m’chigawo cha ku m’mwera cha ku mzambwe a Mavuto M’bobo yomwe ili ku Nyambadwe kuti akabe.

Ofalitsa nkhaniyu wati awiriwa omwe maina awo sakudziwika atalowa mu mpanda wa nyumbayi, anazindikira kuti apolisi amene amalondera nyumbayo awaona ndipo anayamba kulimbana nawo pogwiritsa ntchito zikwanje zomwe ananyamula ndi cholinga choti apeze mpata othawa.

A Sauka anawonjezeraso kuti kulimbanaku kutathina, wapolisi m’modzi anawombera mfuti ndipo chipolopolo chinafikira m’modzi mwa mbava ziwirizi ndipo pomwepo anagwa pansi pamene mzakeyo analiyatsa liwiro la mtondo wadooka, kuthawa.

Oganizilidwa yemwe anawombeledwayo anamwalira pomwe amalandira thandizo la mankhwala pa chipatala cha Queen Elizabeth Central komwe anatengeledwa izi zitachitika.

Apolisi ati pakadali pano akusakasaka achibale a malemuyu komaso ati akusakasaka mbava ina yomwe inathawayo ndipo ngati angagwidwe akuyembekezeka kukayankha mlandu wakuba.

Advertisement