Anthu 12 avulala pa ngozi ku Blantyre

Advertisement

Anthu khumi ndi awiri, avulala pangozi yomwe inachitika ku Kanjedza-Blantyre pamene minibus yomwe adakwera inalowa mbali yolakwika ndikugunda galimoto ya mtundu wa Corolla isanagunde minibus inanso.

Malinga ndi Mneneri wa Polisi ya Limbe, a Aubrey Singanyama, ngoziyi inachitika pafupi ndi malo omwetsela mafuta a Puma ku Blantyre ndipo minibus yomwe inachita ngoziyi imachoka mseu wa Limbe kupita ku Blantyre.

Mneneri yu anati anthuwo anapitisidwa ku chipatala kutsatira ngoziyi ndipo awiri agonekedwa mchipatala pomwe khumi abwerela kunyumba atathandizidwa ndi madotolo.

Oyendetsa galimotoli, a Lenard Jawadi, a zaka 37 amachokera m’mudzi mwa Kabango mfumu yaikulu Kutaja m’boma la Blantyre ndipo azazengedwa mulandu a polisi akamaliza kafukufuku yense.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.