Bambo wafa galimoto yake itaombedwa ndi sitima

Advertisement
Malawi 24 news logo

Bambo wina wa zaka 33, wafa galimoto yomwe amayendetsa momweso munali banja lake itaombedwa ndi sitima ya pa mtunda pa malo owolokera ku Machinga komwe anapita ku tchuthi.

Watsimikiza za nkhaniyi ndi ofalitsa nkhani pa polisi ya Machinga a Western Kansire omwe azindikira malemuwa ngati a Saul Chitseko.

Malingana ndi a Kansire, a Chitseko pamodzi ndi banja lawo lonse anapita ku mudzi kwawo m’boma la Machinga ndi cholinga chokaona abale pa tchuthi cha pasaka kumathero a sabata yatha.

Lolemba pa 1 April, 2024 malemuwa amayendetsa galimoto la mtundu wa KIA yomwe nambala yake ndi MHG 7380 ndipo mu galimotomo munakweraso anthu asanu (5) omwe ndi a pabanja la malemuwa.

Apolisi ati galimotoyi itafika pa malo omwe njanji inawoloka nsewu mdera lotchedwa Mauwa, inaonongeka zomwe zidachititsa kuti iyime mopingasa njanjiyo ndipo pa nthawi yomweyi sitima yonyamula katunduyi inaliso ikubwera kuti iwomboke nsewuwo.

Sitimayi akuti inaomba galimotiyi zomwe zinapangitsa kuti a Chitseko afe ndipo anthu asanu enawo avulale modetsa nkhawa ndipo pano akulandirabe thandizo la mankhwala pa chipatala chachikulu cha Machinga.

Apolisi ati zotsatira za chipatala cha Machinga zasonyeza kuti malemu Chitseko afa kaamba kovulala kwambiri m’mutu mwawo.

Malemuwa anali ochokera m’mudzi mwa Chiwinga kudera la mfumu yaikulu Kawinga m’boma lomweli la Machinga.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.