Bambo wina yemwe dzina lake ndi Mathews Zichepe Banda wa zaka 37 ali mmanja mwa apolisi ku Lingadzi, pomuganizira kuti wakhala akubera anthu a kabaza njinga za kapalasa powamwetsa mankhwala ophera tizilombo otchedwa boric acid ku Lilongwe.
Malingana ndi Mneneri wa polisi ya Lingadzi, Cassim Manda, pa 25 March cha m’ma 9 koloko m’mawa, mkuluyu anapempha wa kabaza wina kuti amutenge kuchoka ku Area 18A kukafika kwa Njewa, ndipo akalipira ndalama yokwana K5000.
“Atafika kumaloko, a Banda anapatsa wakabaza yo chakumwa cha Frozy, ndipo atamwa anayamba kumva chizungulire ndi kukomoka. Apa woganiziridwayo ati anatenga njingayo ndi kukaigulitsa ku Mtandire pamtengo wa K30 000, koma adalandirako kaye K7000,” atero a Manda.
Kutsatira izi, woberedwayo anakamang’ala ku polisi omwe adafufuza ndikupeza njingayo.
A Manda anaonjezera kunena kuti pa 28 March chaka chino woganiziridwayu adapanganso hayala njinga ina kuti akatenge K23 000 yotsala, uku ali ndi cholinga choti pobwerera akamuberenso wanjinga winayo.
Koma atafika ku maloko, apolisi adamanga a Banda ndipo ati adamupeza ndi botolo muli mankhwala omwe akuganiziridwa kuti ndi ophera tizilombowo ali mthumba.
A Banda amachokera m’mudzi wa Fuku m’boma la Ntcheu.