Bungwe la MHRRC lati dziko lino likuyenera kusintha zinthu zina pankhani yokhudza kuchotsa pakati motetezedwa

Advertisement

Bungwe loona za ufulu wa anthu mdziko muno la Malawi Human Rights Resource Centre (MHRRC) lati dziko la Malawi likuyenera kusintha mwa zina zomwe zimalepheletsa atsikana ndi amayi kupeza nawo thandizo lochotsa pakati motetezedwa.

A Enock Chinkhuntha omwe ndi mkulu wa MHRRC polojekiti ndi omwe anena izi kumaphunziro atolankhani nkhani omwe anachitika dzulo la chisanu ku Gland Palace munzinda wa Mzuzu mu polojekiti yotchedwa Breaking Barriers.

Maphunzirowa anachitika pofuna kuphunzitsa atolankhani kuti ziwathandizire akamalemba nkhani zokhudza ufulu wauchembere wabwino pa nkhani zokhudza kugonana.

Ndipo mwa zina, bungwe la MHRRC linapereka malipoti okhudza polojekitiyi yomwe bungwe la MHRRC likuchita pa nkhani imeneyi.

A Chinkhuntha anati ndizodetsa nkhawa kuti dziko lino lakhala likunyalanyaza pankhani yochotsa pakati motetezedwa kamba ka malamulo omwe akadalipo pakadali pano zomwe zikupangitsa kuti amayi ndi asungwana azitaya miyoyo yochuluka.

Ndipo kafukufuku wa mchaka cha 2023 chokha adaonetsa kuti azimayi okwana 35,000 ndi omwe adachotsa pakati mosatetezeka. Kotero a Chinkhuntha anati mkofunika kuti dziko lino lizindikire za tchutchu wa zankhaniyi ndipo iye anapitilizanso kunena kuti mpofunika kuchitapo kanthu mwa machawi.

Pakadali pano dziko la Malawi limaletsa kuchotsa pakati ndipo mayi amaloledwa kuchotsa pakatipo ngati pakubweretsa chiopsezo pa moyo wake.

Advertisement