Abambo atatu anjatidwa kamba kopha mulamu wawo

Advertisement

Abambo atatu ali m’manja mwa apolisi mu mzinda wa Lilongwe powaganizira kuti adapha ndi kukwilira mwa chinsinsi mulamu wawo a Luciano Masiye a zaka 26.

Malingana ndi mneneli wa Polisi ya Lilongwe a Hastings Chigalu, izi zidachitika m’mudzi mwa Lumwila m’bomali, ndipo a Chigalu atsimikiza kuti atatuwa ndi a Polofesa Posiyano a zaka 24, a Steven Kwalapu a zaka 27 ndi a Azele Kaiteni a zaka 38.

A Chigalu ati bambo ophedwayo banja lake lidatha ndi mchemwali wa oganizilidwawa m’mwezi wa February chaka chomwechino ndi kukwatira mkazi wina, koma mwezi wa March pa 10, ophedwawa a Luciano Masiye adapitanso kwa mkazi wawo wakale kuti akambilane.

Malinga ndi a Chigalu kusamvana kunabuka mu kukambilana kwawo, pamene a Masiye adayamba kusakaza zinthu pakhomopo.

Iwo ati izi zidapangitsa mkaziyo kukuwa kufuna thandizo, pamene achimwene a mayiyu adathamangira ku maloku ndi zikwanje komanso zida zina zomwe akuganizila kuti anavulaza nazo a Masiye mpaka kuwapha.

A Chigalu ati pofuna kubisa zonse abambo atatuwa adanyamula thupi la a Masiye usiku omwewo kukakwilira m’manda a m’mudzimo koma nkhani inafukuka patangotha masiku atatu, ndipo potsatila kafukufuku wa apolisi ndi pamene adamanga koyamba a Azele Kaiteni omwe adakaloza pomwe adakwilira thupilo, pomwe awiri enawo anali atathawa.

Atatuwa akaonekela ku bwalo ka milandu kukayankha mlandu wa kupha.